Genesis 50:11 - Buku Lopatulika11 Ndipo pamene anthu okhala m'dzikomo, Akanani, anaona maliro a m'dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro aakulu a Aejipito: chifukwa chake dzina la pamenepo linatchedwa Abele-Mizraimu, pali tsidya lija la Yordani. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Ndipo pamene anthu okhala m'dzikomo, Akanani, anaona maliro a m'dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro akulu a Aejipito: chifukwa chake dzina la pamenepo linatchedwa Abele-Mizraimu, pali tsidya lija la Yordani. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Tsono nzika za ku Kanani zitaona kulira koteroko ku Atadi kuja, zidati, “Kulira kwa maliro kotereku ndi kwa ku Ejipito.” Nchifukwa chake malowo adaŵatchula kuti Abele-Miziraimu, ali kuvuma kwa Yordani. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Akanaani amene ankakhala ku Goreni ha-Atadi ataona mwambo wa maliro anati, “Aigupto ali ndi mwambo wa maliro a akulu.” Ndi chifukwa chake malo amenewo a pafupi ndi Yorodani amatchedwa Abeli-Mizraimu. Onani mutuwo |