Ndipo Yakobo anati kwa a banja lake, ndi kwa onse amene anali ndi iye, Chotsani milungu yachilendo ili mwa inu, mudziyeretse, ndi kupindula zovala zanu:
Eksodo 19:14 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anatsika m'phiri kunka kwa anthu, nawapatulitsa anthu; natsuka iwo zovala zao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anatsika m'phiri kunka kwa anthu, nawapatulitsa anthu; natsuka iwo zovala zao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose adatsika phiri, nakafika kwa anthuwo, ndipo adaŵayeretsa. Anthuwo adachapadi zovala zao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Mose anatsika phiri lija nafika kwa anthu aja ndi kuwayeretsa. Iwo anachapa zovala zawo. |
Ndipo Yakobo anati kwa a banja lake, ndi kwa onse amene anali ndi iye, Chotsani milungu yachilendo ili mwa inu, mudziyeretse, ndi kupindula zovala zanu:
Inu ndinu akulu a nyumba za makolo a Alevi, mudzipatule inu ndi abale anu omwe, kuti mukatenge ndi kukwera nalo likasa la Yehova Mulungu wa Israele ku malo ndalikonzera.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zovala zao.
dzanja lililonse lisalikhudze, wakulikhudza azimponyatu miyala, kapena kumpyoza; ngakhale choweta ngakhale munthu, zisakhale ndi moyo. Pamene lipenga libanika liu lake azikwera m'phirimo.
zonse zakulola moto, mupititse m'moto, ndipo zidzakhala zoyera; koma muziyeretsenso ndi madzi akusiyanitsa. Koma zonse zosalola moto, muzipititse m'madzi.
Ndipo Davide anayankha wansembeyo, nati naye, Zoonadi tinafulatira akazi monga masiku atatu; chichokere ine, zotengera za anyamatawo zinali zopatulika ungakhale unali ulendo wachabe; koposa kotani nanga zotengera zao zikhala zoyera lero?