Ndipo anamlola Rebeka mlongo wao ndi mlezi wake, amuke pamodzi ndi mnyamata wake wa Abrahamu, ndi anthu ake.
Eksodo 18:27 - Buku Lopatulika Ndipo Mose analola mpongozi wake amuke; ndipo anachoka kunka ku dziko lake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose analola mpongozi wake amuke; ndipo anachoka kunka ku dziko lake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yeteroyo atalaŵirana naye Mose, adabwerera kwao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Mose analola kuti mpongozi wake, Yetero anyamuke kubwerera ku dziko la kwawo. |
Ndipo anamlola Rebeka mlongo wao ndi mlezi wake, amuke pamodzi ndi mnyamata wake wa Abrahamu, ndi anthu ake.
M'mamawa Labani anauka nampsompsona ana ake aamuna ndi aakazi, nawadalitsa: ndipo Labani anachoka, nabwera kumalo kwake.
Pamenepo munthuyo ananyamuka kuchoka, iye ndi mkazi wake wamng'ono ndi mnyamata wake; koma mpongozi wake, atate wa mkaziyo, ananena naye, Tapenya, lapendeka dzuwa, ugone kuno usiku; tapenya lapendekatu dzuwa, ugone kuno, nusekerere mtima wako; nimulawire mamawa kunka ulendo wanu kwanu.
Natuluka iye kumene anakhalako ndi apongozi ake awiri pamodzi naye; nanka ulendo wao kubwerera ku dziko la Yuda.