Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 18:26 - Buku Lopatulika

26 Ndipo anaweruza anthu nthawi zonse; mlandu wakuwakanika amabwera nao kwa Mose, ndi milandu yaing'ono yonse amaweruza okha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndipo anaweruza anthu nthawi zonse; mlandu wakuwakanika amabwera nao kwa Mose, ndi milandu yaing'ono yonse amaweruza okha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 ndipo iwowo ankaweruza anthu nthaŵi zonse. Milandu yovuta yokha ankabwera nayo kwa Mose, koma timilandu ting'onoting'ono ankangomaliza okha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Iwowa ankaweruza anthu nthawi zonse. Milandu yovuta ankabwera nayo kwa Mose, koma yosavuta ankayiweruza okha.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 18:26
8 Mawu Ofanana  

Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Sheba mbiri ya Solomoni yakubukitsa dzina la Yehova, anadza kumuyesera iye ndi miyambi yododometsa.


Ndinali atate wa waumphawi; ndi mlandu wa iye amene sindinamdziwe ndinafunsitsa.


ndipo iwo aweruze milandu ya anthu nthawi zonse; ndipo kudzakhala kuti milandu yaikulu yonse abwere nayo kwa iwe; koma milandu yaing'ono yonse aweruze okha; potero idzakuchepera ntchito, ndi iwo adzasenza nawe.


ndipo mwana wamwamuna wa mkazi Wachiisraele anachitira Dzina mwano, natemberera; ndipo anadza naye kwa Mose. Dzina la mai wake ndiye Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani.


Musamasamalira munthu poweruza mlandu; ang'ono ndi akulu muwamvere chimodzimodzi; musamaopa nkhope ya munthu; popeza chiweruzo ncha Mulungu; ndipo mlandu ukakukanikani mubwere nao kwa ine, ndidzaumva.


Ukakukanikani mlandu pouweruza, ndiwo wakunena zamwazi, kapena zakutsutsana, kapena zakupandana, ndiyo milandu yakutengana m'midzi mwanu; pamenepo muziuka ndi kukwera kunka ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa