Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 16:9 - Buku Lopatulika

Ndipo Mose anati kwa Aroni, Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, Yandikizani pamaso pa Yehova, pakuti anamva madandaulo anu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Mose anati kwa Aroni, Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, Yandikizani pamaso pa Yehova, pakuti anamva madandaulo anu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pamenepo Mose adauza Aroni kuti akauze anthuwo kuti, “Bwerani, mudzaime pamaso pa Chauta chifukwa wamva madandaulo anu onse.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kenaka Mose anawuza Aaroni kuti, “Uza gulu lonse la Aisraeli kuti, ‘Bwerani pamaso pa Yehova pakuti wamva kudandaula kwanu.’ ”

Onani mutuwo



Eksodo 16:9
5 Mawu Ofanana  

Ndipo khamu lonse la ana a Israele linadandaulira Mose ndi Aroni m'chipululu;


ndi m'mawa mwake mudzaona ulemerero wa Yehova, popeza alinkumva mulikudandaulira Yehova; pakuti ife ndife chiyani, kuti mutidandaulira ife?


Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m'mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife chiyani? Simulikudandaulira ife koma Yehova.


Ndileke khamu loipa ili lakudandaula pa Ine kufikira liti? Ndidamva madandaulo a ana a Israele, amene amandidandaulira.


Ndipo Mose anati kwa Kora, Iwe ndi khamu lako lonse mukhale pamaso pa Yehova mawa, iwe ndi iwowa, ndi Aroni;