Ndipo musasiyako kufikira m'mawa; koma yotsalira kufikira m'mamawayo muipsereze ndi moto.
Eksodo 16:19 - Buku Lopatulika Ndipo Mose ananena nao, Palibe munthu asiyeko kufikira m'mawa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose ananena nao, Palibe munthu asiyeko kufikira m'mawa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Mose adaŵauza kuti, “Munthu aliyense asasungeko mpaka m'maŵa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Mose anawawuza kuti, “Wina aliyense asasunge mpaka mmawa.” |
Ndipo musasiyako kufikira m'mawa; koma yotsalira kufikira m'mamawayo muipsereze ndi moto.
Koma sanammvere Mose; ndipo ena anasiyako kufikira m'mawa; koma unagwa mphutsi, nununkha. Ndipo Mose anakwiya nao.
Ndipo ananena nao, Ichi ndi chomwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; chimene muziotcha, otchani, ndi chimene muziphika phikani; ndi chotsala chikukhalireni chosungika kufikira m'mawa.
Usapereka mwazi wa nsembe yanga pamodzi ndi mkate wa chotupitsa; ndi mafuta a madyerero anga asagonamo kufikira m'mawa.
Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.