Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 16:20 - Buku Lopatulika

20 Koma sanammvere Mose; ndipo ena anasiyako kufikira m'mawa; koma unagwa mphutsi, nununkha. Ndipo Mose anakwiya nao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Koma sanammvere Mose; ndipo ena anasiyako kufikira m'mawa; koma unagwa mphutsi, nununkha. Ndipo Mose anakwiya nao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Komabe ena mwa iwowo sadamvere zimene adaanena Mosezo, adasungako mpaka m'maŵa mwake. Koma kutacha, adaona kuti tonseto tagwa mphutsi, ndipo tikununkha. Apo Mose adaŵapsera mtima anthuwo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Komabe ena sanamvere Mose, anasungako mpaka mmawa. Koma mmawa mwake tonse tinali mphutsi zokhazokha. Kotero Mose anawapsera mtima.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 16:20
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Mose ananena nao, Palibe munthu asiyeko kufikira m'mawa.


Ndipo anauola m'mawa ndi m'mawa, yense monga mwa njala yake; popeza likatentha dzuwa umasungunuka.


Ndipo anausunga kufikira m'mawa, monga adalamulira Mose; koma sunanunkhe, ndipo sunagwe mphutsi.


Koma munthuyu Mose ndiye wofatsa woposa anthu onse a padziko lapansi.


Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira chopereka chao; sindinalande bulu wao mmodzi, kapena kuchitira choipa mmodzi wa iwowa.


Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba:


Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere.


Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake.


Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.


Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo; mudzikonzere matumba a ndalama amene sakutha, chuma chosatha mu Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga.


Kwiyani, koma musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyire,


Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa