Eksodo 16:16 - Buku Lopatulika Amenewo ndiwo mau walamulira Yehova, Aoleko yense monga mwa njala yake; munthu mmodzi omeri limodzi, monga momwe muli, yense atengere iwo m'hema mwake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Amenewo ndiwo mau walamulira Yehova, Aoleko yense monga mwa njala yake; munthu mmodzi omeri limodzi, monga momwe muli, yense atengere iwo m'hema mwake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta walamula kuti aliyense mwa inu atole womukwanira kudya, ndiye kuti malita aŵiri pa munthu mmodzi, malinga ndi chiŵerengero cha anthu onse a m'hema mwake.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova walamula kuti, ‘Aliyense atole zomukwanira kudya, malita awiri pa munthu mmodzi molingana ndi chiwerengero cha anthu amene ali mu tenti yanu.’ ” |
Ndipo pamene anayesa ndi omeri, iye amene adaola wambiri sunamtsalire, ndi iye amene adaola pang'ono sunamsowe; yense anaola monga mwa njala yake.