Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 16:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Yehova walamula kuti, ‘Aliyense atole zomukwanira kudya, malita awiri pa munthu mmodzi molingana ndi chiwerengero cha anthu amene ali mu tenti yanu.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

16 Amenewo ndiwo mau walamulira Yehova, Aoleko yense monga mwa njala yake; munthu mmodzi omeri limodzi, monga momwe muli, yense atengere iwo m'hema mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Amenewo ndiwo mau walamulira Yehova, Aoleko yense monga mwa njala yake; munthu mmodzi omeri limodzi, monga momwe muli, yense atengere iwo m'hema mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Chauta walamula kuti aliyense mwa inu atole womukwanira kudya, ndiye kuti malita aŵiri pa munthu mmodzi, malinga ndi chiŵerengero cha anthu onse a m'hema mwake.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 16:16
4 Mawu Ofanana  

Aisraeli anachita zonse anawawuza. Ena anatola zambiri ena zochepa.


Ndipo iwo atayeza ndi muyeso wa malita awiri, iye amene anatola zambiri sizinamutsalireko ndipo amene anatola pangʼono sizinamuchepere. Aliyense anatola zomukwanira kudya.


(Malita awiri amafanana ndi gawo lakhumi la efa).


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa