Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anatulutsa ana a Israele m'dziko la Ejipito, monga mwa makamu ao.
Eksodo 16:1 - Buku Lopatulika Ndipo anachoka ku Elimu, ndi khamu lonse la ana a Israele linalowa m'chipululu cha Sini, ndicho pakati pa Elimu ndi Sinai, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anachoka ku Elimu, ndi khamu lonse la ana a Israele linalowa m'chipululu cha Sini, ndicho pakati pa Elimu ndi Sinai, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake khamu lonse la Aisraele lidayamba ulendo kuchokera ku Elimu, ndipo pa tsiku la 15 la mwezi wachiŵiri atachoka ku Ejipito, adafika ku chipululu cha Sini, chimene chili pakati pa Elimu ndi Sinai. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pambuyo pake gulu lonse la Aisraeli linachoka ku Elimu, ndipo pa tsiku la khumi ndi chisanu mwezi wachiwiri chichokere mʼdziko la Igupto, anafika ku chipululu cha Sini chimene chinali pakati pa Elimu ndi Sinai. |
Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anatulutsa ana a Israele m'dziko la Ejipito, monga mwa makamu ao.
Ndipo mukhale naye chisungire kufikira tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi womwe; ndipo gulu lonse la Israele lizamuphe madzulo.
Ndipo anafika pa Elimu, ndi pamenepo panali akasupe a madzi khumi ndi awiri, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; ndipo anamanga chigono chao pomwepo pamadziwo.
Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka m'chipululu cha Sini, M'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona mu Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu.
Mwezi wachitatu atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito, tsiku lomwelo, analowa m'chipululu cha Sinai.