Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.
Eksodo 15:12 - Buku Lopatulika Mwatambasula dzanja lanu lamanja, nthaka inawameza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mwatambasula dzanja lanu lamanja, nthaka inawameza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mudatambalitsa dzanja lanu lamanja, ndipo nthaka idaŵameza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Munatambasula dzanja lanu lamanja ndipo dziko linawameza. |
Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.
Dzanja lanu lamanja, Yehova, lalemekezedwa ndi mphamvu, dzanja lanu lamanja, Yehova, laphwanya mdani.
Umenewu ndi uphungu wopangira dziko lonse; ndipo ili ndi dzanja lotambasulidwa pa amitundu onse.