Eksodo 14:1 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Chauta adalamula Mose kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yehova anati kwa Mose, |
Lankhula ndi anthu a Israele, kuti abwerere m'mbuyo nagone patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, patsogolo pa Baala-Zefoni; pandunji pake mugone panyanja.
Ndipo anachokera ku Etamu, nayenda nabwerera ku Pihahiroti, ndiko kutsogolo kwake kwa Baala-Zefoni; namanga iwo patsogolo pa Migidoli.
Ndipo ndinatulutsa atate anu mu Ejipito; ndipo munadza kunyanja; koma Aejipito analondola atate anu ndi magaleta ndi apakavalo mpaka ku Nyanja Yofiira.