ndipo akakumbukira mitima yao, ali kudziko kumene anatengedwa ukapolo, nakalapa, nakapembedza Inu m'dziko iwo anawatenga ndende, ndi kuti, Tachimwa, ndipo tachita mphulupulu, tachita moipa;
Eksodo 13:17 - Buku Lopatulika Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolere njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati, Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kunka ku Ejipito. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolere njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati, Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kunka ku Ejipito. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Farao ataŵalola Aisraele kuti apite, Mulungu sadaŵadzeretse njira yopita kwa Afilisti, ngakhale kuti imeneyi inali njira yachidule. Mulungu adati, “Sindifuna kuti anthu ameneŵa adzasinthe maganizo ao nadzabwereranso ku Ejipito, akadzangokumana ndi nkhondo yolimbana nawo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Farao atalola anthu aja kuti atuluke, Mulungu sanawadzeretse njira yodutsa dziko la Afilisti, ngakhale kuti inali yachidule popeza Mulungu anati, “Ngati anthuwa atadzakumana ndi nkhondo angadzakhumudwe ndi kubwerera ku Igupto.” |
ndipo akakumbukira mitima yao, ali kudziko kumene anatengedwa ukapolo, nakalapa, nakapembedza Inu m'dziko iwo anawatenga ndende, ndi kuti, Tachimwa, ndipo tachita mphulupulu, tachita moipa;
nakana kumvera, osakumbukiranso zodabwitsa zanu munazichita pakati pao; koma anaumitsa khosi lao, ndipo m'kupanduka kwao anaika mtsogoleri abwerere kunka ku ukapolo wao; koma Inu ndinu Mulungu wokhululukira, wachisomo, ndi wansoni, wolekereza, ndi wochuluka chifundo; ndipo simunawasiye.
Ndipo pamene Farao anayandikira ana a Israele anatukula maso ao, taonani, Aejipito alinkutsata pambuyo pao; ndipo anaopa kwambiri; ndi ana a Israele anafuulira kwa Yehova.
Koma sikunamkomere Paulo kumtenga iye amene anawasiya nabwerera pa Pamfiliya paja osamuka nao kuntchito.
amene makolo athu sanafune kumvera iye, koma anamkankha achoke, nabwerera m'mbuyo mumtima mwao ku Ejipito,
Koma asadzichulukitsire akavalo iye, kapena kubwereretsa anthu anke ku Ejipito, kuti achulukitse akavalo; popeza Yehova anati nanu, Musamabwereranso njira iyi.
Pamenepo akapitao anenenso kwa anthu, ndi kuti, Munthuyo ndani wakuchita mantha ndi wofumuka mtima? Amuke nabwerere kunyumba kwake, ingasungunuke mitima ya abale ake monga mtima wake.
Ndipo Yehova adzakubwezerani ku Ejipito ndi ngalawa, panjira imene ndinati kwa inu, kuti, Simudzaionanso; ndipo kumeneko mudzadzigulitsa kwa adani anu mukhale akapolo ndi adzakazi; koma palibe wogula inu.
Ndi chikhulupiriro anasiya Ejipito, wosaopa mkwiyo wa mfumu; pakuti anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.
Ndipo tsopano, kalalike m'makutu a anthu, ndi kuti, Aliyense wochita mantha, nanjenjemera, abwerere nachoke paphiri la Giliyadi. Ndipo anabwererako anthu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, natsalako zikwi khumi.