Mulankhule ndi gulu lonse la Israele ndi kuti, Tsiku lakhumi la mwezi uno adzitengere munthu yense mwanawankhosa, monga mwa mabanja a atate ao, mwanawankhosa pabanja.
Eksodo 12:47 - Buku Lopatulika Gulu lonse la Israele lizichita ichi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Msonkhano wonse wa Israele uzichita ichi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mtundu wonse wa Aisraele uzichita mwambo umenewu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Gulu lonse la Israeli lizichita mwambo wachikondwererochi. |
Mulankhule ndi gulu lonse la Israele ndi kuti, Tsiku lakhumi la mwezi uno adzitengere munthu yense mwanawankhosa, monga mwa mabanja a atate ao, mwanawankhosa pabanja.
Ndipo mukhale naye chisungire kufikira tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi womwe; ndipo gulu lonse la Israele lizamuphe madzulo.
Munthu akakhala woyera, wosakhala paulendo, koma akaleka kuchita Paska, amsadze munthuyo kwa anthu a mtundu wake; popeza sanabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, munthuyu asenze kuchimwa kwake.
Ndipo mlendo akakhala mwa inu, nakachitira Yehova Paska, azichita monga mwa lemba la Paska, ndi monga mwa chiweruzo chake; lemba likhale limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo, ndi kwa wobadwa m'dziko.