Yosefe ndipo anati kwa abale ake, Ndilinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isaki, ndi kwa Yakobo.
Eksodo 1:6 - Buku Lopatulika Ndipo anafa Yosefe, ndi abale ake onse, ndi mbadwo uwo wonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anafa Yosefe, ndi abale ake onse, ndi mbadwo uwo wonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yosefe adamwalira, abale ake ndi mbadwo wao wonse uja adamwaliranso. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Yosefe ndi abale ake onse ndiponso mʼbado wawo wonse anamwalira. |
Yosefe ndipo anati kwa abale ake, Ndilinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isaki, ndi kwa Yakobo.
Ndipo anafa Yosefe, anali wa zaka zana limodzi ndi khumi; ndipo anakonza thupi lake ndi mankhwala osungira, ndipo anamuika iye m'bokosi mu Ejipito.
Ndiponso mbadwo uwu wonse unasonkhanidwa kuikidwa kwa makolo ao; nuuka mbadwo wina pambuyo pao; wosadziwa Yehova kapena ntchitoyi adaichitira Israele.