popeza anachita choipa pamaso panga, nautsa mkwiyo wanga chitulukire makolo ao mu Ejipito, mpaka lero lino.
Danieli 9:8 - Buku Lopatulika Yehova, kwa ife kuli manyazi a nkhope yathu, kwa mafumu athu, kwa akalonga athu, ndi kwa makolo athu; pakuti takuchimwirani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ambuye, kwa ife kuli manyazi a nkhope yathu, kwa mafumu athu, kwa akalonga athu, ndi kwa makolo athu; pakuti takuchimwirani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu Yehova, ife ndi mafumu athu, akalonga athu ndi makolo athu tili ndi manyazi chifukwa takuchimwirani. |
popeza anachita choipa pamaso panga, nautsa mkwiyo wanga chitulukire makolo ao mu Ejipito, mpaka lero lino.
koma akalingirira m'mtima mwao kudziko kumene anawatengera andende, nakatembenuka, nakapembedzera Inu m'dziko la undende wao, ndi kuti, Tachimwa, tachita mphulupulu, tachita choipa;
mutchere khutu, ndi maso anu atseguke kumvera pemphero la kapolo wanu, ndilipempha pamaso panu tsopano apa msana ndi usiku, kupempherera ana a Israele akapolo anu, ndi kuwulula zoipa za ana a Israele zimene tachimwira nazo Inu; inde tachimwa, ine ndi nyumba ya atate wanga.
Pakuti kuyambira kale anthu sanamve pena kumvetsa ndi khutu, ngakhale diso silinaone Mulungu wina popanda Inu, amene amgwirira ntchito iye amene amlindirira Iye.
Tivomereza, Yehova, chisalungamo chathu, ndi choipa cha makolo athu; pakuti takuchimwirani Inu.
chifukwa cha zoipa zonse za ana a Israele ndi za ana a Yuda, zimene anandiputa nazo Ine, iwowo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, aneneri ao, ndi anthu a Yuda, ndi okhala mu Yerusalemu.
Yehova ali wolungama; pakuti ndapikisana ndi m'kamwa mwake; mumvetu, mitundu ya anthu nonsenu, nimuone chisoni changa; anamwali ndi anyamata anga atha kulowa m'ndende.
kuti uzikumbukira ndi kuchita manyazi ndi kusatsegulanso pakamwa pako konse, chifukwa chamanyazi ako, pamene ndikufafanizira zonse unazichita, ati Ambuye Yehova.
Koma anakaniza maweruzo anga ndi kuchita zoipa koposa amitundu, nakaniza malemba anga koposa maiko akuzungulira; pakuti anataya maweruzo anga, ndi malemba anga, sanayendemo.