Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 9:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Inu Yehova, ife ndi mafumu athu, akalonga athu ndi makolo athu tili ndi manyazi chifukwa takuchimwirani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

8 Yehova, kwa ife kuli manyazi a nkhope yathu, kwa mafumu athu, kwa akalonga athu, ndi kwa makolo athu; pakuti takuchimwirani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ambuye, kwa ife kuli manyazi a nkhope yathu, kwa mafumu athu, kwa akalonga athu, ndi kwa makolo athu; pakuti takuchimwirani.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 9:8
15 Mawu Ofanana  

chifukwa anachita zoyipa pamaso panga ndipo akhala akundikwiyitsa kuchokera tsiku limene makolo awo anatuluka mu Igupto mpaka lero lino.’ ”


Ngati asintha mitima yawo ku dziko limene ali akapolo ndi kulapa ndi kukudandaulirani inu mʼdziko la ukapolo wawo ndi kunena kuti, ‘Ife tachimwa, tachita zolakwa ndipo tachita moyipa kwambiri.’


Tcherani khutu lanu ndi kutsekula maso anu kuti mumve pemphero la mtumiki wanune limene ndikupemphera usana ndi usiku pamaso panu kupempherera Aisraeli, atumiki anu. Ndikuvomereza machimo a Aisraeli amene tinakuchimwirani. Ndithu, ine ndi banja la makolo anga tinakuchimwirani.


Chikhalire palibe ndi mmodzi yemwe anamvapo kapena kuona Mulungu wina wonga Inu, amene amachitira zinthu zotere amene amadikira pa Iye.


Inu Yehova, ife tikuvomereza kuyipa kwathu ndiponso kulakwa kwa makolo athu; ndithu ife tinakuchimwiranidi.


Aisraeli ndi Ayuda, anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu, mafumu awo, nduna zawo, ansembe ndi aneneri awo anandikwiyitsa ndi ntchito zawo zoyipa.


Koma kodi akuvutitsa Ine? Kodi sakungodzivuta okha, ndi kudzichititsa manyazi? akutero Yehova.”


“Yehova ndi wolungama, koma ndine ndinawukira malamulo ake. Imvani inu anthu a mitundu yonse; onani masautso anga. Anyamata ndi anamwali anga agwidwa ukapolo.


“Ife tachimwa ndi kuwukira ndipo inu simunakhululuke.


Chipewa chathu chaufumu chagwa pamutu pathu. Tsoka kwa ife, chifukwa tachimwa!


Ndikadzakukhululukira zoyipa zako zonse zimene unachita, udzazikumbukira ndipo udzachita manyazi kwambiri, kotero kuti sudzatha nʼkuyankhula komwe, akutero Ambuye Yehova.’ ”


Koma anthu a Yerusalemu aphwanya malamulo anga pochita zoyipa kuposa anthu a mitundu ina. Iwo anandipandukira kupambana anthu ena amene awazungulira. Iwo anakana malamulo anga ndipo sanasunge malangizo anga.


Ambuye Mulungu wathu ndi wachifundo ndi wokhululuka, ngakhale kuti tamuwukira:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa