Yeremiya 32:32 - Buku Lopatulika32 chifukwa cha zoipa zonse za ana a Israele ndi za ana a Yuda, zimene anandiputa nazo Ine, iwowo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, aneneri ao, ndi anthu a Yuda, ndi okhala mu Yerusalemu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201432 chifukwa cha zoipa zonse za ana a Israele ndi za ana a Yuda, zimene anandiputa nazo Ine, iwowo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, aneneri ao, ndi anthu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa32 Aisraele ndi Ayuda, mafumu ao, akalonga, ansembe, aneneri, pamodzi ndi onse okhala ku Yerusalemu ndi ku Yuda, adandikwiyitsa ndi ntchito zao zoipa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero32 Aisraeli ndi Ayuda, anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu, mafumu awo, nduna zawo, ansembe ndi aneneri awo anandikwiyitsa ndi ntchito zawo zoyipa. Onani mutuwo |
Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tinkachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa.