Ndipo pakuuka iye ufumu wake udzathyoledwa, nudzagawikira kumphepo zinai za mlengalenga; koma sadzaulandira a mbumba yake akudza m'mbuyo, kapena monga mwa ulamuliro wake anachita ufumu nao; pakuti ufumu wake udzazulidwa, ukhale wa ena, si wa aja ai.
Danieli 8:22 - Buku Lopatulika Ndi kuti zinaphuka zinai m'malo mwake mwa iyo itathyoka, adzauka maufumu anai ochokera mu mtunduwu wa anthu, koma osakhala nayo mphamvu ya uja. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi kuti zinaphuka zinai m'malo mwake mwa iyo itathyoka, adzauka maufumu anai ochokera mu mtunduwu wa anthu, koma osakhala nayo mphamvu ya uja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kunena za nyanga inathyoka ija ndi nyanga zinayi zimene zinaphuka mʼmalo mwake zikutanthauza maufumu anayi amene adzatuluka mʼdziko lake; koma sizidzafanana mphamvu ndi ufumu woyambawo. |
Ndipo pakuuka iye ufumu wake udzathyoledwa, nudzagawikira kumphepo zinai za mlengalenga; koma sadzaulandira a mbumba yake akudza m'mbuyo, kapena monga mwa ulamuliro wake anachita ufumu nao; pakuti ufumu wake udzazulidwa, ukhale wa ena, si wa aja ai.
Pambuyo pake ndinapenya ndi kuona china ngati nyalugwe, chinali nao mapiko anai a nkhuku pamsana pake, chilombocho chinali nayonso mitu inai, napatsidwa ulamuliro.
Pambuyo pake ndinaona m'masomphenya a usiku, ndi kuona chilombo chachinai, choopsa ndi chochititsa mantha, ndi champhamvu choposa, chinali nao mano aakulu achitsulo, chinalusa ndi kuphwanya ndi kupondereza chotsala ndi mapazi ake; chinasiyana ndi zilombo zonse zidachitsogolera; ndipo chinali ndi nyanga khumi.
Ndi tonde wamanyenje ndiye mfumu ya Agriki, ndi nyanga yaikulu ili pakati pamaso ake ndiyo mfumu yoyamba.
Ndipo potsiriza pake pa ufumu wao, atakwanira olakwa, idzauka mfumu ya nkhope yaukali yakuzindikira zinsinsi.
Ndipo ndinakweza maso anga ndi kupenya; taonani, panaima pamtsinje nkhosa yamphongo yokhala nazo nyanga ziwiri, ndi nyanga ziwirizo zinali za msinkhu wautali, koma imodzi inaposa inzake; yoposayo inaphuka m'mbuyo.
Ndipo tondeyo anadzikulitsa kwakukulu, koma atakhala wamphamvu, nyanga yake yaikulu inathyoka; ndi m'malo mwake munaphuka nyanga zinai zooneka bwino, zoloza kumphepo zinai za mlengalenga.
Ndipo ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anatuluka magaleta anai pakati pa mapiri awiri; ndi mapiriwo ndiwo mapiri amkuwa.