Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 8:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo tondeyo anadzikulitsa kwakukulu, koma atakhala wamphamvu, nyanga yake yaikulu inathyoka; ndi m'malo mwake munaphuka nyanga zinai zooneka bwino, zoloza kumphepo zinai za mlengalenga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo tondeyo anadzikulitsa kwakukulu, koma atakhala wamphamvu, nyanga yake yaikulu inathyoka; ndi m'malo mwake munaphuka nyanga zinai zooneka bwino, zoloza kumphepo zinai za mlengalenga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mbuziyo inayamba kudzikuza kwambiri chifukwa cha mphamvu zake koma pamene mphamvuzo zinakula kwambiri nyanga yake yayikulu inathyoka, ndipo mʼmalo mwake panamera nyanga zinayi moloza mbali zonse zinayi.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 8:8
19 Mawu Ofanana  

Koma atakhala wamphamvu, mtima wake unakwezeka momuononga, nalakwira Yehova Mulungu wake; popeza analowa mu Kachisi wa Yehova kufukiza paguwa la nsembe la chofukiza.


Pakuti Mordekai anali wamkulu m'nyumba ya mfumu, ndi mbiri yake idabuka m'maiko onse; pakuti munthuyu Mordekai anakulakulabe.


Pa Elamu ndidzatengera mphepo zinai kumbali zinai za mlengalenga, ndidzamwaza iwo kumphepo zonsezo; ndipo sikudzakhala mtundu kumene opirikitsidwa a Elamu sadzafikako.


Monga chikwere chodzala ndi mbalame, chomwecho nyumba zao zadzala ndi chinyengo; chifukwa chake akula, alemera.


Ndinakuchulukitsa ngati mphundu za kumunda; ndipo unathululuka ndi kukula kufikira wakongola nkhope, mawere ako anamera, ndi tsitsi lako linamera; koma unali wamaliseche ndi wausiwa.


Kodi udzanena ndithu pamaso pa iye wakupha iwe, Ine ndine Mulungu, pokhala uli munthu, wosati Mulungu, m'dzanja la iye wakupha iwe.


Ndipo pakuuka iye ufumu wake udzathyoledwa, nudzagawikira kumphepo zinai za mlengalenga; koma sadzaulandira a mbumba yake akudza m'mbuyo, kapena monga mwa ulamuliro wake anachita ufumu nao; pakuti ufumu wake udzazulidwa, ukhale wa ena, si wa aja ai.


Akali m'kamwa mwa mfumu mau awa, anamgwera mau ochokera kumwamba, ndi kuti, Mfumu Nebukadinezara, anena kwa iwe: ufumu wakuchokera.


Koma pokwezeka mtima wake, nulimba mzimu wake kuchita modzikuza, anamtsitsa pa mpando wa ufumu wake, namchotsera ulemerero wake;


Daniele ananena, nati, Ndinaona m'masomphenya anga usiku, taonani, mphepo zinai za mumlengalenga zinabuka pa nyanja yaikulu.


Pambuyo pake ndinapenya ndi kuona china ngati nyalugwe, chinali nao mapiko anai a nkhuku pamsana pake, chilombocho chinali nayonso mitu inai, napatsidwa ulamuliro.


Ndi kuti zinaphuka zinai m'malo mwake mwa iyo itathyoka, adzauka maufumu anai ochokera mu mtunduwu wa anthu, koma osakhala nayo mphamvu ya uja.


Ndipo polingirirapo ine, taonani, wadza tonde wochokera kumadzulo, pa nkhope ya dziko lonse lapansi, wosakhudza nthaka; ndi mbuziyo inali ndi nyanga yooneka bwino pakati pamaso ake.


Ndipo ndinamuona wayandikira pafupi pa nkhosa yamphongo, nawawidwa mtima nayo, naigunda nkhosa yamphongo, nathyola nyanga zake ziwiri; ndipo mphongoyo inalibe mphamvu yakuima pamaso pake, koma anaigwetsa pansi, naipondereza; ndipo panalibe wakupulumutsa mphongoyo m'dzanja lake.


Ndipo Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kumphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena.


Ndipo pamenepo adzatuma angelo, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake ochokera kumphepo zinai, kuyambira ku malekezero ake a dziko lapansi, ndi kufikira ku malekezero a thambo.


Pakuti nditakalowetsa awa m'dziko limene ndinalumbirira makolo ao, moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ndipo atadya nakhuta, nanenepa, pamenepo adzatembenukira milungu ina, ndi kuitumikira, ndi kundipeputsa Ine, ndi kuthyola chipangano changa.


Zitatha izi ndinaona angelo anai alinkuimirira pangodya zinai za dziko, akugwira mphepo zinai za dziko, kuti ingaombe mphepo padziko, kapena panyanja, kapena pa mtengo uliwonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa