Danieli 8:22 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 Kunena za nyanga inathyoka ija ndi nyanga zinayi zimene zinaphuka mʼmalo mwake zikutanthauza maufumu anayi amene adzatuluka mʼdziko lake; koma sizidzafanana mphamvu ndi ufumu woyambawo. Onani mutuwoBuku Lopatulika22 Ndi kuti zinaphuka zinai m'malo mwake mwa iyo itathyoka, adzauka maufumu anai ochokera mu mtunduwu wa anthu, koma osakhala nayo mphamvu ya uja. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 Ndi kuti zinaphuka zinai m'malo mwake mwa iyo itathyoka, adzauka maufumu anai ochokera mu mtunduwu wa anthu, koma osakhala nayo mphamvu ya uja. Onani mutuwo |
“Zitatha izi, mʼmasomphenya anga usiku, ndinaonanso chirombo chachinayi chitayima patsogolo panga. Chinali choopsa, chochititsa mantha ndi champhamvu kwambiri. Chinali ndi mano akuluakulu a chitsulo. Chimati chikatekedza ndi kumeza adani ake kenaka chinapondereza chilichonse chotsala. Ichi chinali chosiyana ndi zirombo zoyambirira zija, ndipo chinali ndi nyanga khumi.