Ndipo linalinkulowa dzuwa, ndi tulo tatikulu tinamgwera Abramu: ndipo taonani, kuopsa kwa mdima waukulu kunamgwera iye.
Danieli 8:18 - Buku Lopatulika Ndipo m'mene analikulankhula ndi ine ndinagwidwa ndi tulo tatikulu, nkhope yanga pansi; koma anandikhudza, nandiimiritsa pokhala inepo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'mene analikulankhula ndi ine ndinagwidwa ndi tulo tatikulu, nkhope yanga pansi; koma anandikhudza, nandiimiritsa pokhala inepo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene ankandiyankhula ndinadzigwetsa pansi chafufumimba, nʼkugona tulo tofa nato. Kenaka anandikhudza ndi kundiyimiritsa. |
Ndipo linalinkulowa dzuwa, ndi tulo tatikulu tinamgwera Abramu: ndipo taonani, kuopsa kwa mdima waukulu kunamgwera iye.
Ndipo unandilowa mzimu pamene ananena nane, ndi kundiimika ndikhale chilili; ndipo ndinamumva Iye wakunena nane.
Ndipo taonani, wina wakunga ana a anthu anakhudza milomo yanga; pamenepo ndinatsegula pakamwa panga ndi kunena naye woima popenyana nane, Mbuye wanga, chifukwa cha masomphenyawo zowawa zanga zandibwerera, ndipo ndilibenso mphamvu.
Nayandikira iye poima inepo; atadza iye tsono ndinachita mantha, ndinagwa nkhope pansi; koma anati kwa ine, Zindikira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti masomphenyawo anena za nthawi ya chimaliziro.
Ndipo ine Daniele ndinakomoka ndi kudwala masiku ena; pamenepo ndinauka ndi kuchita ntchito ya mfumu; ndipo ndinadabwa nao masomphenyawo, koma panalibe wakuwazindikiritsa.
Ndipo mthengayo adalankhula nane, anadzanso, nandiutsa ngati munthu woutsidwa m'tulo take.
Ndipo pamene ananyamuka pakupemphera anadza kwa ophunzira, nawapeza ali m'tulo ndi chisoni,
Koma Petro ndi iwo anali naye analemedwa ndi tulo; koma m'mene anayera m'maso ndithu, anaona ulemerero wake, ndi amuna awiriwo akuimirira ndi Iye.
Ndipo tsopano ndiimirira pano ndiweruzidwe pa chiyembekezo cha lonjezano limene Mulungu analichita kwa makolo athu;
Ndipo pamene ndinamuona Iye, ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lake lamanja pa ine, nati, Usaope, Ine ndine Woyamba ndi Wotsiriza,