Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 9:32 - Buku Lopatulika

32 Koma Petro ndi iwo anali naye analemedwa ndi tulo; koma m'mene anayera m'maso ndithu, anaona ulemerero wake, ndi amuna awiriwo akuimirira ndi Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Koma Petro ndi iwo anali naye analemedwa ndi tulo; koma m'mene anayera m'maso ndithu, anaona ulemerero wake, ndi amuna awiriwo akuimirira ndi Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Nthaŵi imeneyo nkuti Petro ndi anzake ali m'tulo tofa nato. Koma pamene adadzuka, adaona ulemerero wa Yesu, ndiponso anthu aŵiri aja ali naye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Petro ndi anzake anali ndi tulo tambiri, koma atadzuka, iwo anaona ulemerero wake ndi anthu awiri atayima pamodzi ndi Iye.

Onani mutuwo Koperani




Luka 9:32
13 Mawu Ofanana  

Dzuwa silidzakhalanso kuunika kwako usana, ngakhale mwezi sudzakuunikiranso kuti kuyere; koma Yehova adzakhala kwa iwe kuunika kosatha, ndi Mulungu wako adzakhala ulemerero wako.


Ndipo ndinamva kunena kwa mau ake, ndipo pamene ndinamva kunena kwa mau ake ndinagwidwa ndi tulo tatikulu pankhope panga, nkhope yanga pansi.


Ndipo m'mene analikulankhula ndi ine ndinagwidwa ndi tulo tatikulu, nkhope yanga pansi; koma anandikhudza, nandiimiritsa pokhala inepo.


Ndipo anadzanso nawapeza ali m'tulo, pakuti maso ao analemeradi; ndipo sanadziwe chomyankha Iye.


Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.


Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi.


Pakuti sitinatsate miyambi yachabe, pamene tinakudziwitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu, koma tinapenya m'maso ukulu wake.


Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa