Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 9:33 - Buku Lopatulika

33 Ndipo panali polekana iwo aja ndi Iye, Petro anati kwa Yesu, Ambuye, nkwabwino kuti tili pano; ndipo timange misasa itatu, umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya; wosadziwa iye chimene alikunena.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Ndipo panali polekana iwo aja ndi Iye, Petro anati kwa Yesu, Ambuye, nkwabwino kuti tili pano; ndipo timange misasa itatu, umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya; wosadziwa iye chimene alikunena.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Pamene iwo aja ankalekana naye, Petro adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, ndi bwino kuti ife tili nao pano. Tiloleni timange misasa itatu, wina wanu, wina wa Mose, wina wa Eliya.” (Sankadziŵa zimene ankanena.)

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Pamene anthuwo ankamusiya Yesu, Petro anati kwa Iye, “Ambuye, ndi chabwino kwa ife kuti tikhale pano. Tiloleni kuti timange misasa itatu, umodzi wanu, umodzi wa Mose ndi umodzi wa Eliya.” (Iye sanadziwe chimene amayankhula).

Onani mutuwo Koperani




Luka 9:33
13 Mawu Ofanana  

Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.


Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu. Ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.


Ndipo pamene iwo anadza kukhamu la anthu, kunafika kwa Iye munthu, namgwadira Iye, nati,


Ndipo Petro anayankha, nati kwa Yesu, Ambuye, kuli bwino kuti ife tikhale pano; ngati mulola ndidzamanga pano misasa itatu; umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.


Koma Yesu anati kwa iwo, Simudziwa chimene muchipempha. Mukhoza kodi kumwera chikho chimene ndimwera Ine? Kapena kubatizidwa ndi ubatizo umene ndibatizidwa nao Ine?


Ndipo Simoni anayankha, nati, Ambuye, tinagwiritsa ntchito usiku wonse osakola kanthu, koma pa mau anu ndidzaponya makoka.


Ndipo akadalankhula izi, unadza mtambo, nuwaphimba iwo; ndipo anaopa pakulowa iwo mumtambo.


Ndipo Yohane anayankha nati, Ambuye, tinaona wina alikutulutsa ziwanda m'dzina lanu; ndipo tinamletsa, chifukwa satsatana nafe.


Filipo ananena ndi Iye, Ambuye, tionetsereni ife Atate, ndipo chitikwanira.


Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa