Danieli 5:27 - Buku Lopatulika TEKEL, Mwayesedwa pamiyeso, nimupezeka mwaperewera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 TEKEL, Mwayesedwa pamiyeso, nimupezeka mwaperewera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tekeli: Inu mwayesedwa pa sikelo ndipo mwapezeka kuti mukuperewera. |
Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu aakulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya.
Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, udzitengere mpeni wakuthwa, ndiwo lumo la wometa, udzitengere ndi kulipititsa pamutu pako ndi pa ndevu zako; nudzitengere muyeso kuyesa nao, ndi kugawa tsitsilo.
Ndipo Yehova walamulira za iwe kuti asabzalidwenso ena a dzina lako; m'nyumba ya milungu yako ndidzachotsa fano losema ndi fano loyenga; ndidzakukonzerapo manda, pakuti iwe ndiwe wopepuka.
ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbululuka m'moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani.