Koma sanadzichepetse pamaso pa Yehova, monga umo anadzichepetsera Manase atate wake; koma Amoni amene anachulukitsa kupalamula kwake.
Danieli 5:22 - Buku Lopatulika Ndipo inu mwana wake, Belisazara inu, simunadzichepetse m'mtima mwanu, chinkana munazidziwa izi zonse; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo inu mwana wake, Belisazara inu, simunadzichepetsa m'mtima mwanu, chinkana munazidziwa izi zonse; Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Koma inu mwana wake, Belisazara, simunadzichepetse, ngakhale kuti mumadziwa zonsezi. |
Koma sanadzichepetse pamaso pa Yehova, monga umo anadzichepetsera Manase atate wake; koma Amoni amene anachulukitsa kupalamula kwake.
nachita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wake; sanadzichepetse kwa Yeremiya mneneri wakunena zochokera pakamwa pa Yehova.
Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;
Ndipo ndidzalanga dziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao, ndi oipa chifukwa cha mphulupulu zao; ndipo ndidzaletsa kudzikuza kwa onyada, ndidzagwetsa kudzikweza kwa oopsa.
Ndipo iwe unati mumtima mwako, Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba paphiri la khamu, m'malekezero a kumpoto;
Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira chilungamo; m'dziko la machitidwe oongoka, iye adzangochimwa, sadzaona chifumu cha Yehova.
Mfumu inu, Mulungu Wam'mwambamwamba anapatsa Nebukadinezara atate wanu ufumuwu, ndi ukulu, ndi ulemerero, ndi chifumu;
Popeza Yohane anadza kwa inu m'njira ya chilungamo, ndipo simunamvere iye; koma amisonkho ndi akazi achiwerewere anammvera iye; ndipo inu, m'mene munachiona, simunalape pambuyo pake, kuti mumvere iye.
Ndipo kapolo uyo, wodziwa chifuniro cha mbuye wake, ndipo sanakonze, ndi kusachita zonga za chifuniro chakecho, adzakwapulidwa mikwapulo yambiri.
Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.