Mateyu 21:32 - Buku Lopatulika32 Popeza Yohane anadza kwa inu m'njira ya chilungamo, ndipo simunamvere iye; koma amisonkho ndi akazi achiwerewere anammvera iye; ndipo inu, m'mene munachiona, simunalape pambuyo pake, kuti mumvere iye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201432 Popeza Yohane anadza kwa inu m'njira ya chilungamo, ndipo simunamvera iye; koma amisonkho ndi akazi achiwerewere anammvera iye; ndipo inu, m'mene munachiona, simunalapa pambuyo pake, kuti mumvere iye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa32 Paja Yohane Mbatizi adaabwera nadzakuwonetsani njira ya chilungamo, inu osamkhulupirira, m'menemo okhometsa msonkho ndi akazi adama adamkhulupirira. Inuyo ngakhale mudaziwona zimenezo, simudasinthe maganizo pambuyo pake kuti muzimkhulupirira.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero32 Pakuti Yohane anabwera kwa inu kuti akuonetseni njira yachilungamo, koma inu simunakhulupirire iye, koma amisonkho ndi adama anamukhulupirira. Koma ngakhale munaona izi, simunatembenuke mtima ndi kumukhulupirira iye. Onani mutuwo |