Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 21:31 - Buku Lopatulika

31 Ndani wa awiriwo anachita chifuniro cha atate wake? Iwo ananena, Woyambayo. Yesu ananena kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti amisonkho ndi akazi achiwerewere amatsogolera inu, kulowa mu Ufumu wa Kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Ndani wa awiriwo anachita chifuniro cha atate wake? Iwo ananena, Woyambayo. Yesu ananena kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti amisonkho ndi akazi achiwerewere amatsogolera inu, kulowa mu Ufumu wa Kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Kodi mwa aŵiriwo, yemwe adachita zimene bambo wake ankafuna ndi uti?” Iwo adati, “Woyamba uja.” Yesu adaŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti okhometsa msonkho ndi akazi adama akuloŵa mu Ufumu wa Mulungu inu nkumakusiyani m'mbuyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 “Ndani wa awiriwa anachita chimene abambo ake amafuna?” Anamuyankha nati, “Woyambayo.” Yesu anawawuza kuti, “Ndikuwuzani zoonadi, kuti amisonkho ndi adama akulowa mu ufumu wa Mulungu inu musanalowemo.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 21:31
26 Mawu Ofanana  

Pakamwa pako pakutsutsa, si ine ai. Inde milomo yako ikuchitira umboni wakukutsutsa.


Uziti nao, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israele?


Pakuti aliyense amene adzachita chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amai wanga.


nati, Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.


Chomwecho omalizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omalizira.


Ndipo anadza kwa winayo, natero momwemo. Ndipo iye anavomera, nati, Ndipita mbuye; koma sanapite.


Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kake kamodzi sikadzachokera kuchilamulo, kufikira zitachitidwa zonse.


Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho?


Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; chifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m'masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.


Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.


Ndipo Yesu popita, kuchokera kumeneko, anaona munthu, dzina lake Mateyu, alinkukhala polandirira msonkho, nanena kwa iye, Nditsate Ine. Ndipo iye anauka, namtsata.


Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.


Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula chimene sindinachiike, ndi wotuta chimene sindinachifese;


Ndipo anthu onse ndi amisonkho omwe, pakumva, anavomereza kuti Mulungu ali wolungama, popeza anabatizidwa iwo ndi ubatizo wa Yohane.


Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sangathe kuona Ufumu wa Mulungu.


Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sangathe kulowa ufumu wa Mulungu.


Nthawi za kusadziwako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponseponse atembenuke mtima;


Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;


Ndipo lamulo linalowa moonjezera, kuti kulakwa kukachuluke; koma pamene uchimo unachuluka, pomwepo chisomo chinachuluka koposa;


Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa