Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 21:33 - Buku Lopatulika

33 Mverani fanizo lina: Panali munthu, mwini banja, amene analima munda wampesa, nauzunguniza linga, nakumba umo moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Mverani fanizo lina: Panali munthu, mwini banja, amene analima munda wamphesa, nauzunguniza linga, nakumba umo moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Yesu adati, “Imvani fanizo lina. Munthu wina anali ndi munda wake. M'mundamo adaabzalamo mipesa, namanga mpanda kuzinga mundawo. Adakumba nkhuti yoponderamo mphesa, namanga nsanja yolondera mundawo. Pambuyo pake munda uja adaubwereka alimi, iye nkunyamuka ulendo wa ku dziko lina.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 “Tamverani fanizo lina: Panali mwini munda amene anadzala mphesa. Anamanga mpanda kuzungulira mundawo, nakumba moponderamo mphesa ndipo anamanga nsanja. Kenaka anabwereketsa munda wamphesawo kwa alimi ena napita pa ulendo.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 21:33
23 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Chifukwa chake tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lili chilili m'mbali mwake, ku dzanja lamanja ndi lamanzere.


Imvani mau a Yehova inu olamulira a Sodomu, tcherani makutu ku chilamulo cha Mulungu wathu, inu anthu a Gomora.


nuti, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi okhala mu Yerusalemu; Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzatengera malo ano choipa, chimene aliyense adzachimva, makutu ake adzachita woo.


Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pake, ya mpesa wachilendo?


Imvani mau a Yehova, inu ana a Israele; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi okhala m'dziko, popeza palibe choonadi, kapena chifundo, kapena kudziwa Mulungu m'dziko.


Ndipo tsono mverani inu fanizolo la wofesa mbeu uja.


Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu mwini banja, amene anatuluka mamawa kukalembera antchito a m'munda wake wampesa.


Nanga mutani? Munthu anali nao ana awiri; nadza iye kwa woyamba nati, Mwanawe, kagwire lero ntchito kumunda wampesa.


nanena, Alembi ndi Afarisi akhala pa mpando wa Mose;


Monga ngati munthu wa paulendo, adachoka kunyumba kwake, nawapatsa akapolo ake ulamuliro, kwa munthu aliyense ntchito yake, nalamula wapakhomo adikire.


Pamenepo anati, Munthu wa fuko lomveka ananka kudziko lakutali, kudzilandirira yekha ufumu, ndi kubwerako.


Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam'munda.


Mudziikire oweruza ndi akapitao m'midzi yanu yonse imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, monga mwa mafuko anu; ndipo aweruze anthu ndi chiweruzo cholungama.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa