Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 5:2 - Buku Lopatulika

Belisazara, pakulawa vinyo, anati abwere nazo zotengera za golide ndi siliva adazichotsa Nebukadinezara atate wake ku Kachisi ali ku Yerusalemu, kuti mfumu ndi akulu ake, akazi ake ndi akazi ake aang'ono, amweremo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Belisazara, pakulawa vinyo, anati abwere nazo zotengera za golide ndi siliva adazichotsa Nebukadinezara atate wake ku Kachisi ali ku Yerusalemu, kuti mfumu ndi akulu ake, akazi ake ndi akazi ake ang'ono, amweremo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Pamene Belisazara ankamwa vinyo, analamula kuti ziwiya zagolide ndi zasiliva zimene Nebukadinezara abambo ake anakatenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu zikatengedwe kuti mfumu ndi akalonga ake, akazi ake ndi azikazi amweremo.

Onani mutuwo



Danieli 5:2
23 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakuchitira kukoma mtima chifukwa cha Yonatani atate wako; ndi minda yonse ya Saulo ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa chikhalire.


Natulutsa kuchotsa komweko chuma chonse cha nyumba ya Yehova, ndi chuma cha nyumba ya mfumu, naduladula zipangizo zonse zagolide adazipanga Solomoni mfumu ya Israele mu Kachisi wa Yehova, monga Yehova adanena.


Ndi zopalira moto, ndi mbale zowazira za golide yekhayekha, ndi zasiliva yekhayekha, mkulu wa asilikali anazichotsa.


Ndi pambuyo pake anatenga Maaka mwana wamkazi wa Abisalomu; ndipo anambalira Abiya, ndi Atai, ndi Ziza, ndi Selomiti.


Maaka yemwe, mai wake wa Asa, mfumu, namchotsa uyu asakhalenso mai wa ufumu, popeza anapanga fanizo lolaula; ndipo Asa analikha fanizolo, naliphwanyaphwanya, nalitenthera ku mtsinje wa Kidroni.


Ndipo pofikanso nyengo, mfumu Nebukadinezara anatumiza anthu abwere naye ku Babiloni, pamodzi ndi zipangizo zokoma za nyumba ya Yehova; nalonga Zedekiya mbale wake mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.


Ndi zipangizo zonse za nyumba ya Mulungu, zazikulu ndi zazing'ono, ndi chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma cha mfumu, ndi cha akalonga ake, anabwera nazo zonsezi ku Babiloni.


Ndiponso zipangizo za golide ndi siliva za nyumba ya Mulungu, anazitulutsa Nebukadinezara mu Kachisi anali ku Yerusalemu, ndi kubwera nazo ku Kachisi wa ku Babiloni, izizo Kirusi mfumu anazitulutsa mu Kachisi wa ku Babiloni, nazipereka kwa munthu dzina lake Sezibazara, amene anamuika akhale kazembe;


Ndipo amitundu onse adzamtumikira iye, ndi mwana wake, ndi mdzukulu wake, mpaka yafika nthawi ya dziko lake; ndipo amitundu ambiri ndi mafumu aakulu adzamuyesa iye mtumiki wao.


Lupanga lili pa Ababiloni, ati Yehova, pa okhala mu Babiloni, pa akulu ake, ndi pa anzeru ake.


Ndi zikho, ndi zopalira moto, ndi mbale, ndi miphika, ndi zoikaponyali, ndi zipande, ndi mitsuko; ndi golide, wa zija zagolide, ndi siliva, wa zija zasiliva, kapitao wa alonda anazichotsa.


Ndipo Ambuye anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda, m'dzanja lake, pamodzi ndi zipangizo zina za m'nyumba ya Mulungu, namuka nazo iye kudziko la Sinara, kunyumba ya mulungu wake, nalonga zipangizozo m'nyumba ya chuma cha mulungu wake.


pali munthu mu ufumu mwanu mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera; ndipo masiku a atate wanu munapezeka mwa iye kuunika, ndi luntha, ndi nzeru, ngati nzeru ya milungu; ndipo mfumu Nebukadinezara atate wanu, inde mfumu atate wanu anamuika akhale mkulu wa alembi, openda, Ababiloni, ndi alauli;


Pamenepo analowa naye Daniele kwa mfumu. Mfumu inayankha, niti kwa Daniele, Ndiwe kodi Daniele uja wa ana a ndende a Yuda, amene mfumu atate wanga anatenga ku Yuda?


Mfumu inu, Mulungu Wam'mwambamwamba anapatsa Nebukadinezara atate wanu ufumuwu, ndi ukulu, ndi ulemerero, ndi chifumu;


koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu aang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitire ulemu.


Nabwera nazo zotengera zagolide adazichotsa ku Kachisi wa nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemu, ndipo mfumu ndi akulu ake, akazi ake ndi akazi ake aang'ono, anamweramo.


Usiku womwewo Belisazara mfumu ya Ababiloni anaphedwa.


Anamwa vinyo, nalemekeza milungu yagolide, ndi yasiliva, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala.


chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosakaniza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;