Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 7:79 - Buku Lopatulika

79 chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosakaniza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

79 chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

79 Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

79 Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lowazira lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika, zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya;

Onani mutuwo Koperani




Numeri 7:79
5 Mawu Ofanana  

zikho zagolide makumi atatu, zikho zasiliva zina mazana anai ndi khumi, zipangizo zina chikwi chimodzi.


Kuwerenga kwake ndiko: mbale zagolide makumi atatu, mbale zasiliva chikwi chimodzi, mipeni makumi awiri mphambu isanu ndi inai;


Belisazara, pakulawa vinyo, anati abwere nazo zotengera za golide ndi siliva adazichotsa Nebukadinezara atate wake ku Kachisi ali ku Yerusalemu, kuti mfumu ndi akulu ake, akazi ake ndi akazi ake aang'ono, amweremo.


chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;


Ndipo iye, atampangira amake, anati, Ndipatseni ine kuno m'mbale mutu wa Yohane Mbatizi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa