Danieli 5:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Pamene Belisazara ankamwa vinyo, analamula kuti ziwiya zagolide ndi zasiliva zimene Nebukadinezara abambo ake anakatenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu zikatengedwe kuti mfumu ndi akalonga ake, akazi ake ndi azikazi amweremo. Onani mutuwoBuku Lopatulika2 Belisazara, pakulawa vinyo, anati abwere nazo zotengera za golide ndi siliva adazichotsa Nebukadinezara atate wake ku Kachisi ali ku Yerusalemu, kuti mfumu ndi akulu ake, akazi ake ndi akazi ake aang'ono, amweremo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Belisazara, pakulawa vinyo, anati abwere nazo zotengera za golide ndi siliva adazichotsa Nebukadinezara atate wake ku Kachisi ali ku Yerusalemu, kuti mfumu ndi akulu ake, akazi ake ndi akazi ake ang'ono, amweremo. Onani mutuwo |
Ndipo ziwiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara anazitenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu ndi kukaziyika mʼnyumba ya milungu ya ku Babuloni, anakazichotsa ku nyumba ya milungu ya ku Babuloniko ndi kuzipereka kwa Sesibazara, amene mfumu inamusankha kukhala bwanamkubwa.
Pali munthu wina mu ufumu wanu uno amene mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera. Pa nthawi ya ulamuliro wa abambo anu iye anapezeka kuti ali ndi chidziwitso, luntha ndi nzeru zonga za milungu. Mfumu Nebukadinezara, abambo anu, Ine ndikukuwuzani anamusankha iye kukhala mkulu wa amatsenga, owombeza, alawuli ndi amawula.
Mʼmalo mwake, mwadzikweza nokha kutsutsana ndi Ambuye wakumwamba. Inu mwatenga ziwiya za mʼNyumba mwake, ndipo inu ndi akalonga anu, akazi anu ndi azikazi anu mwamwera vinyo mu zimenezi. Inu munatamanda milungu yasiliva ndi golide, yamkuwa, chitsulo, mtengo ndi mwala, imene singaone kapena kumva kapena kuzindikira. Koma simunamupatse ulemu Mulungu amene asunga mʼmanja mwake moyo wanu ndi njira zanu zonse.