Danieli 5:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Choncho anabweretsa ziwiya zagolide zimene anazitenga mʼNyumba ya Mulungu; ndipo mfumu ndi akalonga ake, akazi ake ndi azikazi ake anamweramo. Onani mutuwoBuku Lopatulika3 Nabwera nazo zotengera zagolide adazichotsa ku Kachisi wa nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemu, ndipo mfumu ndi akulu ake, akazi ake ndi akazi ake aang'ono, anamweramo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Nabwera nazo zotengera zagolide adazichotsa ku Kachisi wa nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemu, ndipo mfumu ndi akulu ake, akazi ake ndi akazi ake ang'ono, anamweramo. Onani mutuwo |
Mʼmalo mwake, mwadzikweza nokha kutsutsana ndi Ambuye wakumwamba. Inu mwatenga ziwiya za mʼNyumba mwake, ndipo inu ndi akalonga anu, akazi anu ndi azikazi anu mwamwera vinyo mu zimenezi. Inu munatamanda milungu yasiliva ndi golide, yamkuwa, chitsulo, mtengo ndi mwala, imene singaone kapena kumva kapena kuzindikira. Koma simunamupatse ulemu Mulungu amene asunga mʼmanja mwake moyo wanu ndi njira zanu zonse.