Danieli 4:28 - Buku Lopatulika Chonsechi chinagwera mfumu Nebukadinezara. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chonsechi chinagwera mfumu Nebukadinezara. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zonsezi zinamuchitikira mfumu Nebukadinezara. |
Koma pokwezeka mtima wake, nulimba mzimu wake kuchita modzikuza, anamtsitsa pa mpando wa ufumu wake, namchotsera ulemerero wake;
Koma mau anga ndi malemba anga, amene ndinalamulira atumiki anga aneneriwo, kodi sanawapeze makolo anu? Ndipo anabwera, nati, Monga umo Yehova wa makamu analingirira kutichitira ife, monga mwa njira zathu ndi monga mwa machitidwe athu, momwemo anatichitira.
Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?