Zekariya 1:6 - Buku Lopatulika6 Koma mau anga ndi malemba anga, amene ndinalamulira atumiki anga aneneriwo, kodi sanawapeze makolo anu? Ndipo anabwera, nati, Monga umo Yehova wa makamu analingirira kutichitira ife, monga mwa njira zathu ndi monga mwa machitidwe athu, momwemo anatichitira. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Koma mau anga ndi malemba anga, amene ndinalamulira atumiki anga aneneriwo, kodi sanawapeze makolo anu? Ndipo anabwera, nati, Monga umo Yehova wa makamu analingirira kutichitira ife, monga mwa njira zathu ndi monga mwa machitidwe athu, momwemo anatichitira. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Kodi mau anga ndi malamulo anga amene ndidauza atumiki anga aneneri, suja adamveka kwa makolo anu? Choncho iwo adalapa ndi kunena kuti, ‘Chauta Wamphamvuzonse watichitadi zomwe adaatsimikiza kuti adzatichita, potsata makhalidwe athu ndi ntchito zathu zoipa.’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Kodi mawu anga ndi malangizo anga, amene ndinawawuza atumiki anga aneneri, suja anawachitira makolo anu? “Tsono iwo analapa ndi kunena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse watichitira zomwe zikuyenera njira zathu ndi machitidwe athu, monga anatsimikiza kuti adzachita.’ ” Onani mutuwo |