Pamenepo mzimu unavala Amasai, ndiye wamkulu wa makumi atatuwo, nati iye, Ndife anu, Davide, tivomerezana nanu mwana wa Yese inu: mtendere, mtendere ukhale ndi inu, ndi mtendere ukhale ndi athandizi anu; pakuti Mulungu wanu akuthandizani. Ndipo Davide anawalandira, nawaika akulu a magulu.