Babiloni wakhala chikho chagolide m'dzanja la Yehova, amene analedzeretsa dziko lonse lapansi; amitundu amwa vinyo wake; chifukwa chake amitundu ali ndi misala.
Danieli 3:7 - Buku Lopatulika Potero nthawi yomweyo pakumva anthu onse mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ndi zoimbitsa zilizonse, anthu onse, mitundu ya anthu a manenedwe osiyana, anagwadira, nalambira fano lagolide adaliimika mfumu Nebukadinezara. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Potero nthawi yomweyo pakumva anthu onse mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ndi zoimbitsa zilizonse, anthu onse, mitundu ya anthu a manenedwe osiyana, anagwadira, nalambira fano lagolide adaliimika mfumu Nebukadinezara. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho anthu onse aja atangomva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, analambira ndi kupembedza fano la golide limene mfumu Nebukadinezara analiyimika. |
Babiloni wakhala chikho chagolide m'dzanja la Yehova, amene analedzeretsa dziko lonse lapansi; amitundu amwa vinyo wake; chifukwa chake amitundu ali ndi misala.
Pamenepo mfumu Nebukadinezara anagwa nkhope yake pansi, nalambira Daniele, nati amthirire nsembe yaufa ndi ya zonunkhira zokoma.
Inu mfumu mwalamulira kuti munthu aliyense amene adzamva mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, agwadire, nalambire fanolo lagolide;
Ndipo wolalikira anafuulitsa, kuti, Akulamulirani inu anthu, mitundu ya anthu a manenedwe osiyana,
kuti pakumva inu mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, mugwadire ndi kulambira fano lagolide adaliimika mfumu Nebukadinezara;
ndipo aliyense wosagwadira ndi kulambira, adzaponyedwa nthawi yomweyo m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.
Tidziwa kuti tili ife ochokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.
Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.
Ndipo chisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikiro zimene anachipatsa mphamvu yakuzichita pamaso pa chilombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fano la chilombocho, chimene chinali nalo bala la lupanga ndi kukhalanso ndi moyo.
Ndipo umodzi wa mitu yake unakhala ngati unalasidwa kufikira imfa; ndipo bala lake la kuimfa lidapola; ndipo dziko lonse linazizwa potsata chilombocho;
Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi.
Chilombo chimene unachiona chinaliko, koma kulibe; ndipo chidzatuluka m'chiphompho chakuya, ndi kunka kuchitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo chiyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona chilombo, kuti chinaliko, ndipo kulibe, ndipo chidzakhalako.
Ndipo chinagwidwa chilombocho, ndi pamodzi nacho mneneri wonyenga amene adachita zizindikiro pamaso pake, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la chilombo, ndi iwo akulambira fano lake; iwo awiri anaponyedwa ali moyo m'nyanja yamoto yakutentha ndi sulufure: