Yeremiya 51:7 - Buku Lopatulika7 Babiloni wakhala chikho chagolide m'dzanja la Yehova, amene analedzeretsa dziko lonse lapansi; amitundu amwa vinyo wake; chifukwa chake amitundu ali ndi misala. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Babiloni wakhala chikho chagolide m'dzanja la Yehova, amene analedzeretsa dziko lonse lapansi; amitundu amwa vinyo wake; chifukwa chake amitundu ali ndi misala. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Pajatu Babiloni anali ngati chikho chagolide m'manja mwa Chauta, kuti aledzeretse dziko lonse lapansi. Mitundu yambiri ya anthu idamwako vinyo wake, nchifukwa chake idapenga. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Babuloni anali ngati chikho cha golide mʼdzanja la Yehova; kuti aledzeretse dziko lonse lapansi. Mitundu yambiri ya anthu inamwa vinyo wake; nʼchifukwa chake tsopano inachita misala. Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.