Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 51:8 - Buku Lopatulika

8 Babiloni wagwa dzidzidzi naonongedwa; mumkuwire iye; mutengere zowawa zake vunguti, kapena angachire.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Babiloni wagwa dzidzidzi naonongedwa; mumkuwire iye; mutengere zowawa zake vunguti, kapena angachire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Babiloni wagwa mwadzidzidzi ndipo waonongeka. Mlireni, mfunireni mankhwala, kuti mwina nkuchira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Babuloni wagwa mwadzidzidzi ndi kusweka. Mulireni! Mfunireni mankhwala opha ululu wake; mwina iye nʼkuchira.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 51:8
20 Mawu Ofanana  

ndipo taonani, kuno kulinkudza khamu la amuna, apakavalo awiriawiri. Ndipo iye anayankha nati, Babiloni wagwa, wagwa; ndi mafano onse osema a milungu yake asweka, nagwa pansi.


Chifukwa chake choipa chidzafika pa iwe; sudzadziwa kucha kwake, ndipo chionongeko chidzakugwera; sudzatha kuchikankhira kumbali; ndipo chipasuko chosachidziwa iwe chidzakugwera mwadzidzidzi.


koma izi ziwiri zidzakugwera mwadzidzidzi, tsiku limodzi kumwalira kwa ana ndi umasiye zidzakugwera; mokwanira monse, pakati pa maphenda ako ambirimbiri.


Kwera ku Giliyadi, tenga vunguti, namwali iwe mwana wa Ejipito; wachulukitsa mankhwala chabe; palibe kuchira kwako.


Mowabu wachitidwa manyazi, pakuti wathyoka; kuwa nulire, nunene mu Arinoni, kuti Mowabu wapasuka.


Chifukwa chake ndidzakuwira Mowabu; inde, ndidzafuulira Mowabu yense, adzalirira anthu a ku Kiriheresi.


Lalikirani mwa amitundu, falikitsani, kwezani mbendera; falikitsani, musabise; munene, Babiloni wagwidwa, Beli wachitidwa manyazi, Merodaki wathyokathyoka, zosema zake zachitidwa manyazi, mafano ake athyokathyoka.


Sesaki wagwidwatu! Chimene dziko lonse lapansi linachitamanda chalandidwa dzidzidzi! Babiloni wakhalatu bwinja pakati pa amitundu!


Kodi mulibe vunguti mu Giliyadi? Kodi mulibe sing'anga m'menemo; analekeranji kuchira mwana wamkazi wa anthu anga?


Wobadwa ndi munthu iwe, nenera, uziti, Atero Ambuye Yehova, Liritsani, Ha, tsikulo!


Pamenepo nsonga ya dzanja inatumidwa kuchokera pamaso pake, nililembedwa lembali.


Ndipo Dariusi Mmedi analandira ufumuwo ali wa zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri.


Palibe chakulunzitsa kuthyoka kwako; bala lako liwawa; onse akumva mbiri yako akuombera manja; pakuti ndaniyo kuipa kwako sikunampitapitabe?


Ndipo anatsata mngelo wina mnzake ndi kunena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu umene unamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake.


Ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu, nusandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa