Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 51:9 - Buku Lopatulika

9 Tikadachiritsa Babiloni koma sanachire; mumsiye iye, tipite tonse yense kudziko lake; pakuti chiweruziro chake chifikira kumwamba, chinyamulidwa mpaka kuthambo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Tikadachiritsa Babiloni koma sanachire; mumsiye iye, tipite tonse yense kudziko lake; pakuti chiweruziro chake chifikira kumwamba, chinyamulidwa mpaka kuthambo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ena adati, ‘Tidayesa kumpatsa mankhwala koma sadachire. Tiyeni tingomsiya, timchokere ndipo aliyense apite ku dziko lakwao. Paja mlandu wake wafika mpaka kumwamba, wafika mpaka ku mlengalenga.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ena anati, “ ‘Ife tinayesa kumupatsa mankhwala Babuloni, koma sanachire; tiyeni timusiye ndipo aliyense apite ku dziko la kwawo, pakuti mlandu wake wafika mpaka mlengalenga, wafika mpaka kumwamba.’

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 51:9
13 Mawu Ofanana  

Koma panali mneneri wa Yehova pomwepo, dzina lake Odedi; natuluka iye kukomana nayo nkhondo ikudzayo ku Samariya, nanena nao, Taonani, popeza Yehova Mulungu wa makolo anu anakwiya ndi Yuda, anawapereka m'dzanja lanu, nimunawapha ndi kupsa mtima kofikira kumwamba.


ndipo ndinati, Mulungu wanga, ndigwa nkhope, ndi kuchita manyazi kuweramutsa nkhope yanga kwa inu Mulungu wanga, popeza mphulupulu zathu zachuluka pamutu pathu, ndi kupalamula kwathu kwakula kufikira mu Mwamba.


Ndipo padzakhala kuti monga mbawala yothamangitsidwa, ndi monga nkhosa zosazisonkhanitsa anthu, adzatembenukira yense kwa anthu ake, nathawira yense kudziko lake.


Zinthu zomwe unagwira ntchito yake, zidzatero nawe; iwo amene anachita malonda ndi iwe chiyambire pa ubwana wako, adzayenda yense kunka kumalo kwake; sipadzakhala wopulumutsa iwe.


Anaphunthwitsa ambiri, inde, anagwa wina pa mnzake, ndipo anati, Ukani, tinkenso kwa anthu athu, kudziko la kubadwa kwathu, kuchokera kulupanga lovutitsa.


Ndiponso olipidwa ake ali pakati pake onga ngati anaang'ombe a m'khola; pakuti iwonso abwerera, athawa pamodzi, sanaime; pakuti tsiku la tsoka lao linawafikira, ndi nthawi ya kuweruzidwa kwao.


Muwathe ofesa ku Babiloni, ndi iwo amene agwira chisenga nyengo ya masika; chifukwa cha lupanga losautsa adzatembenukira yense kwa anthu ake, nadzathawira yense ku dziko lake.


Masika apita, mphakasa yatha, ndipo ife sitinapulumutsidwe.


Tsoka kwa iwowa! Pakuti anandizembera; chionongeko kwa iwowa! Pakuti anandilakwira; ndikadawalanditsa Ine, koma anandinenera zabodza.


Ndipo ndinamva mau ena ochokera Kumwamba, nanena, Tulukani m'menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake;


pakuti machimo ake anaunjikizana kufikira mu Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa