Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 51:10 - Buku Lopatulika

10 Yehova watulutsa chilungamo chathu; tiyeni tilalikire mu Ziyoni ntchito ya Yehova Mulungu wathu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Yehova watulutsa chilungamo chathu; tiyeni tilalikire m'Ziyoni ntchito ya Yehova Mulungu wathu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Tsono Chauta waonetsa poyera kuti ifeyo ndife osalakwa. Tiyeni tilengeze ku Ziyoni zimene Chauta, Mulungu wathu, watichitira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 “ ‘Yehova waonetsa poyera kuti ndife osalakwa; tiyeni tilengeze mu Ziyoni zimene Yehova Mulungu wathu wachita.’

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 51:10
18 Mawu Ofanana  

Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo, ndipo ndidzafotokozera ntchito za Yehova.


Ndipo adzaonetsa chilungamo chako monga kuunika, ndi kuweruza kwako monga usana.


Ndipo anthu onse adzachita mantha; nadzabukitsa chochita Mulungu, nadzasamalira ntchito yake.


Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu, ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga.


Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse; pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni, ndidzakondwera nacho chipulumutso chanu.


Amenewa adzakweza mau ao, nadzafuula; chifukwa cha chifumu cha Yehova, iwo adzafuula zolimba panyanja.


Munene inu zotonthoza mtima kwa Yerusalemu, nimufuulire kwa iye, kuti nkhondo yake yatha, kuti kuipa kwake kwakhululukidwa; kuti iye walandira mowirikiza m'dzanja la Yehova, chifukwa cha machimo ake onse.


Ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni; ndi nyimbo ndi kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; adzakhala m'kusangalala ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.


Mau a iwo akuthawa akupulumuka m'dziko la Babiloni, kuti alalikire mu Ziyoni kubwezera chilango kwa Yehova Mulungu wathu, kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake.


Chifukwa chake tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Babiloni; ndi zimene walingirira dziko la Ababiloni; ndithu adzawakoka, ana aang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa