Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 3:23 - Buku Lopatulika

Ndipo amuna atatu awa, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, anagwa pansi omangidwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo amuna atatu awa, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, anagwa pansi omangidwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

ndipo anyamata atatuwa, ali chimangidwire, anagwera mʼngʼanjo ya moto.

Onani mutuwo



Danieli 3:23
13 Mawu Ofanana  

Masautso a wolungama mtima achuluka, koma Yehova amlanditsa mwa onsewa.


Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.


Ndipo anatenga Yeremiya, namponya iye m'dzenje la Malikiya mwana wake wa mfumu, limene linali m'bwalo la kaidi; ndipo anamtsitsa Yeremiya ndi zingwe. Koma m'dzenjemo munalibe madzi, koma thope; namira Yeremiya m'thopemo.


Ndi mkulu wa adindo anawapatsa maina ena; Daniele anamutcha Belitesazara; ndi Hananiya, Sadrake; ndi Misaele, Mesaki; ndi Azariya, Abedenego.


Pamenepo mfumu Nebukadinezara anadabwa, nauka msanga, nanena nati kwa mandoda ake, Kodi sitinaponye amuna atatu omangidwa m'kati mwa moto? Anayankha nati kwa mfumu, Inde mfumu.


Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero;


nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa, analimbikitsidwa pokhala ofooka, anakula mphamvu kunkhondo, anapirikitsa magulu a nkhondo yachilendo.