Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 3:24 - Buku Lopatulika

24 Pamenepo mfumu Nebukadinezara anadabwa, nauka msanga, nanena nati kwa mandoda ake, Kodi sitinaponye amuna atatu omangidwa m'kati mwa moto? Anayankha nati kwa mfumu, Inde mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Pamenepo mfumu Nebukadinezara anadabwa, nauka msanga, nanena nati kwa mandoda ake, Kodi sitinaponya amuna atatu omangidwa m'kati mwa moto? Anayankha nati kwa mfumu, Inde mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Kenaka mfumu Nebukadinezara anadabwa ndipo anafunsa nduna zake kuti, “Kodi sanali amuna atatu amene anamangidwa ndi kuponyedwa mʼmoto?” Iwo anayankha kuti, “Ndi zoonadi, mfumu.”

Onani mutuwo Koperani




Danieli 3:24
18 Mawu Ofanana  

Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga umo anachitira a nyumba ya Ahabu; pakuti ompangira ndi iwowa, atamwalira atate wake; ndi kuonongeka kwake nkumeneko.


Taonani, Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m'ng'anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m'dzanja lanu, mfumu.


Ndipo amuna atatu awa, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, anagwa pansi omangidwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.


Anayankha, nati, Taonani, ndilikuona amuna anai omasuka, alikuyenda m'kati mwa moto; ndipo alibe kuphwetekwa, ndi maonekedwe a wachinai akunga mwana wa milungu.


ndinu, mfumu; mwakula, mwalimba, pakuti ukulu wanu wakula, nufikira kumwamba, ndi ufumu wanu ku chilekezero cha dziko lapansi.


Chifukwa chake, mfumu, kupangira kwanga kukomere inu, dulani machimo anu ndi kuchita chilungamo, ndi mphulupulu zanu mwa kuchitira aumphawi chifundo; kuti kapena nthawi ya mtendere wanu italike.


Mfumu inu, Mulungu Wam'mwambamwamba anapatsa Nebukadinezara atate wanu ufumuwu, ndi ukulu, ndi ulemerero, ndi chifumu;


Pamenepo padasandulika pa nkhope pake pa mfumu, ndi maganizo ake anamsautsa, ndi mfundo za m'chuuno mwake zinaguluka, ndi maondo ake anaombana.


Mulungu wanga watuma mthenga wake, natseka pakamwa pa mikango; ndipo siinandipweteka, chifukwa anandiona wosachimwa pamaso pake, pamaso panunso, mfumu, sindinalakwe.


Akulu onse a ufumuwo, ndi akazembe ndi akalonga, mandoda, ndi ziwanga, anapangana kukhazika lemba lachifumu, ndi kuikapo choletsa cholimba, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango.


Ndipo m'mene anagogoda pa chitseko cha pakhomo, anadza kudzavomera mdzakazi, dzina lake Roda.


dzuwa lamsana, ndinaona panjira, Mfumu, kuunika kochokera kumwamba kowalitsa koposa dzuwa kunawala pondizinga ine ndi iwo akundiperekeza.


Mfumu Agripa, mukhulupirira aneneri kodi? Ndidziwa kuti muwakhulupirira.


komatu, uka, nulowe m'mzinda, ndipo kudzanenedwa kwa iwe chimene uyenera kuchita.


Ndipo pamene Saulo anaona Davide alikutulukira kwa Mfilistiyo, iye anati kwa Abinere, kazembe wa khamu la nkhondo, Abinere, mnyamata uyu ndi mwana wa yani? Nati Abinere, Pali moyo wanu, mfumu, ngati ndidziwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa