Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 38:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo anatenga Yeremiya, namponya iye m'dzenje la Malikiya mwana wake wa mfumu, limene linali m'bwalo la kaidi; ndipo anamtsitsa Yeremiya ndi zingwe. Koma m'dzenjemo munalibe madzi, koma thope; namira Yeremiya m'thopemo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo anatenga Yeremiya, namponya iye m'dzenje la Malikiya mwana wake wa mfumu, limene linali m'bwalo la kaidi; ndipo anamtsitsa Yeremiya ndi zingwe. Koma m'dzenjemo munalibe madzi, koma thope; namira Yeremiya m'thopemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Choncho iwo aja adatenga Yeremiya, nakamponya m'chitsime chimene adaakumba Malakiya mwana wa mfumu, m'bwalo la alonda a mfumu. Adamtsitsira m'menemo ndi chingwe. M'chitsimemo munalibe madzi, munali matope okhaokha. Ndipo Yeremiya adamira m'matopemo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Choncho iwo anatenga Yeremiya nakamuponya mʼchitsime cha Malikiya, mwana wa mfumu, chimene chinali mʼbwalo la alonda. Iwo anamutsitsira mʼdzenjemo ndi chingwe. Munalibe madzi koma matope okhaokha, ndipo Yeremiya anamira mʼmatopewo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 38:6
19 Mawu Ofanana  

ndipo anamtenga iye, namponya m'dzenjemo; m'dzenjemo munalibe kanthu, munalibe madzi m'menemo.


Ndipo anandisenza choipa m'malo mwa chokoma, ndi udani m'malo mwa chikondi changa.


Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko, ndi m'thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.


Ndamira m'thope lozama, lopanda poponderapo; ndalowa m'madzi ozama, ndipo chigumula chandimiza.


Nthawi yomweyo nkhondo ya mfumu ya Babiloni inamangira Yerusalemu misasa; ndipo Yeremiya mneneri anatsekeredwa m'bwalo la kaidi, linali kunyumba ya mfumu ya Yuda.


Ndipo mfumu inauza Yerameele mwana wake wa mfumu, ndi Seraya mwana wa Aziriele, ndi Selemiya mwana wa Abideele, kuti awagwire Baruki mlembi ndi Yeremiya mneneri; koma Yehova anawabisa.


Atafika Yeremiya kunyumba yadzenje, ku tizipinda take nakhalako Yeremiya masiku ambiri;


Ndipo Zedekiya mfumu analamula, ndipo anamuika Yeremiya m'bwalo la kaidi, tsiku ndi tsiku, nampatsa mkate wofuma kumseu wa oumba mikate, mpaka unatha mkate wonse wa m'mzinda. Ndipo Yeremiya anakhala m'bwalo la kaidi.


Ndipo anamkweza Yeremiya ndi zingwe, namtulutsa m'dzenjemo; ndipo Yeremiya anakhalabe m'bwalo la kaidi.


Taonani, akazi onse otsala m'nyumba ya mfumu ya Yuda adzatulutsidwa kunka kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, ndipo akaziwo adzati, Oyanjana nanu anakunyengani, ndi kukuposani inu, mapazi anu amire m'thope, abwerera m'mbuyo.


Pamenepo inalamula mfumu, ndipo anadza naye Daniele, namponya m'dzenje la mikango. Ndipo mfumu inalankhula, niti kwa Daniele, Mulungu wako amene umtumikira kosalekeza, Iyeyu adzakulanditsa.


Iwenso, chifukwa cha mwazi wa pangano lako ndinatulutsa andende ako m'dzenje m'mene mulibe madzi.


Pakumva iye kulamulira kotero anawaika m'chipinda cha m'kati, namangitsa mapazi ao m'zigologolo.


Pakuti chikusowani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa