Namuka iye, napeza mtembo wake wogwera m'njira, ndi bulu ndi mkango zili chiimire pafupi ndi mtembo. Mkango udalibe kudya mtembo, kapena kukadzula bulu.
Danieli 3:22 - Buku Lopatulika Motero, popeza mau a mfumu anafulumiza, ndi ng'anjo inatentha koposa, lawi la moto linapha iwo aja ananyamula Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Motero, popeza mau a mfumu anafulumiza, ndi ng'anjo inatentha koposa, lawi la moto linapha iwo aja ananyamula Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono popeza lamulo la mfumu linali lofulumiza, ngʼanjo inatenthetsedwa kowirikiza mwakuti malawi ake anapha asilikali amene ananyamula Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, |
Namuka iye, napeza mtembo wake wogwera m'njira, ndi bulu ndi mkango zili chiimire pafupi ndi mtembo. Mkango udalibe kudya mtembo, kapena kukadzula bulu.
Ndipo Aejipito anaumiriza anthuwo, nafulumira kuwatulutsa m'dziko; pakuti anati, Tili akufa tonse.
Wochimwa ndiye chiombolo cha wolungama; ndipo wachiwembu adzalowa m'malo mwa oongoka mtima.
Ndi mkulu wa adindo anawapatsa maina ena; Daniele anamutcha Belitesazara; ndi Hananiya, Sadrake; ndi Misaele, Mesaki; ndi Azariya, Abedenego.
anayankha nati kwa Ariyoki mkulu wa olindirira a mfumu, Chilamuliro cha mfumu chifulumiriranji? Pamenepo Ariyoki anadziwitsa Daniele chinthuchi.
Ndipo italamulira mfumu, anabwera nao amuna aja adamneneza Daniele, nawaponya m'dzenje la mikango, iwowa, ana ao, ndi akazi ao; ndipo asanafike pansi pa dzenje mikango inawaposa mphamvu, niphwanya mafupa ao onse.
Ndipo pamene Herode adamfunafuna, wosampeza, anafunsitsa odikira nalamulira aphedwe. Ndipo anatsika ku Yudeya kunka ku Kesareya, nakhalabe kumeneko.