Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 6:24 - Buku Lopatulika

24 Ndipo italamulira mfumu, anabwera nao amuna aja adamneneza Daniele, nawaponya m'dzenje la mikango, iwowa, ana ao, ndi akazi ao; ndipo asanafike pansi pa dzenje mikango inawaposa mphamvu, niphwanya mafupa ao onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndipo italamulira mfumu, anabwera nao amuna aja adamneneza Daniele, nawaponya m'dzenje la mikango, iwowa, ana ao, ndi akazi ao; ndipo asanafike pansi pa dzenje mikango inawaposa mphamvu, niphwanya mafupa ao onse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Mwa lamulo la mfumu, anthu onse amene ananeneza Danieli aja anagwidwa ndi kukaponyedwa mʼdzenje la mikango, pamodzi ndi akazi awo ndi ana awo. Ndipo asanafike pansi pa dzenjelo, mikango inawawakha ndi mphamvu ndi kuteketa mafupa awo onse.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 6:24
13 Mawu Ofanana  

koma ana a ambandawo sanawaphe, monga mwalembedwa m'buku la chilamulo cha Mose, m'mene adalamulira Yehova, ndi kuti, Atate asaphedwere ana, kapena ana kuphedwera atate; koma yense afere kulakwa kwa iye yekha.


Nampachika Hamani pa mtengo adaukonzera Mordekai. Pamenepo mkwiyo wa mfumu unatsika.


ana aamuna khumi a Hamani mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda. Koma sanalande zofunkha.


koma pofika mlanduwo kwa mfumu, iye adalamula polemba kalata kuti chiwembu choipa cha Hamani adachipangira Ayuda chimbwerere mwini; ndi kuti iye ndi ana ake aamuna apachikidwe pamtengo.


Adzabwezera choipa adani anga, aduleni m'choonadi chanu.


Wolungama apulumuka kuvuto; woipa nalowa m'malo mwake.


Mboni yonama sidzapulumuka chilango; wolankhula mabodza adzaonongeka.


Ndinadzitonthoza kufikira mamawa; monga mkango, momwemo Iye anathyolathyola mafupa anga onse; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.


Chifukwa chake Yehova atero: Simunandimvere Ine, kuti mulalikire ufulu, munthu yense kwa mbale wake, ndi munthu yense kwa mnzake; taonani, ndilalikira kwa inu ufulu, ati Yehova, wa kulupanga, kumliri, ndi kunjala; ndipo ndidzakuperekani mukhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi.


Motero, popeza mau a mfumu anafulumiza, ndi ng'anjo inatentha koposa, lawi la moto linapha iwo aja ananyamula Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego.


Atate asaphedwere ana, ndi ana asaphedwere atate; munthu yense aphedwere tchimo lakelake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa