Ndipo Davide ananena ndi mkulu wa Alevi kuti aike abale ao oimbawo ndi zoimbira, zisakasa, ndi azeze, ndi nsanje, azimveketse ndi kukweza mau ao ndi chimwemwe.
Danieli 3:10 - Buku Lopatulika Inu mfumu mwalamulira kuti munthu aliyense amene adzamva mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, agwadire, nalambire fanolo lagolide; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inu mfumu mwalamulira kuti munthu aliyense amene adzamva mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, agwadire, nalambire fanolo lagolide; Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mfumu, mwakhazikitsa lamulo kuti aliyense akamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, ayenera kulambira ndi kupembedza fano la golide, |
Ndipo Davide ananena ndi mkulu wa Alevi kuti aike abale ao oimbawo ndi zoimbira, zisakasa, ndi azeze, ndi nsanje, azimveketse ndi kukweza mau ao ndi chimwemwe.
Momwemo Aisraele onse anakwera nalo likasa la chipangano la Yehova ndi kufuula, ndi kumveka kwa lipenga, ndi mphalasa, ndi nsanje zomveketsa, ndi zisakasa, ndi azeze.
Ndipo anaika Alevi m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, monga umo adauzira Davide, ndi Gadi mlauli wa mfumu, ndi Natani mneneriyo; pakuti lamulo ili lidafuma kwa Yehova mwa aneneri ake.
Kodi uyenera kuyanjana ndi Inu mpando wachifumu wa kusakaza, wakupanga chovuta chikhale lamulo?
ninati, Pamene muchiza akazi a Ahebri nimuwaone pamipando; akakhala mwana wamwamuna, mumuphe; akakhala wamkazi, akhale ndi moyo.
Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana aamuna onse akabadwa aponyeni m'mtsinje, koma ana aakazi onse alekeni amoyo.
Ndiponso ndinaona kunja kuno malo akuweruza, komweko kuli zoipa; ndi malo a chilungamo, komweko kuli zoipa.
Mukavomereza tsono, pakumva mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ndi ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, kugwadira ndi kulambira fano ndinalipanga, chabwino; koma mukapanda kulambira, mudzaponyedwa nthawi yomweyi m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto; ndipo mulungu yemwe adzakulanditsani m'manja mwanga ndani?
Ndipo anayandikira, nanena pamaso pa mfumu za choletsacho cha mfumu, Kodi simunatsimikize choletsacho, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense, masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango? Mfumu niyankha, niti, Choona chinthuchi, monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi amene sasinthika.
Koma ansembe aakulu ndi Afarisi adalamula kuti, munthu wina akadziwa pokhala Iye, aulule, kuti akamgwire Iye.