Pamenepo mfumu inasandutsa Daniele wamkulu, nimpatsa mphatso zazikulu zambiri, namlamuliritsa dera lonse la ku Babiloni; nakhala iye kazembe wamkulu wa anzeru onse a ku Babiloni.
Danieli 2:6 - Buku Lopatulika Koma mukandidziwitsa lotoli, ndi kumasulira kwake, mudzalandira kwa ine mphatso, ndi mphotho, ndi ulemu waukulu; chifukwa chake mundidziwitse lotoli ndi kumasulira kwake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma mukandidziwitsa lotoli, ndi kumasulira kwake, mudzalandira kwa ine mphatso, ndi mphotho, ndi ulemu waukulu; chifukwa chake mundidziwitse lotoli ndi kumasulira kwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ngati mundiwuza zimene ndalota ndi tanthauzo lake, ndidzakupatsani mphatso ndi mphotho ndi ulemu waukulu. Choncho mundiwuze zimene ndalota ndi tanthauzo lake.” |
Pamenepo mfumu inasandutsa Daniele wamkulu, nimpatsa mphatso zazikulu zambiri, namlamuliritsa dera lonse la ku Babiloni; nakhala iye kazembe wamkulu wa anzeru onse a ku Babiloni.
Pamenepo Belisazara analamulira, ndipo anaveka Daniele chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwake, nalalikira za iye kuti ndiye wolamulira wachitatu mu ufumumo.
Nifuulitsa mfumu abwere nao openda, Ababiloni, ndi alauli. Mfumu inalankhula, niti kwa anzeru a ku Babiloni, Aliyense amene adzawerenga lemba ili, nadzandifotokozera kumasulira kwake, adzavekedwa chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwake, nadzakhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.
popeza ndidzakuchitira ulemu waukulu, ndipo zonse unena ndi ine ndidzachita; chifukwa chake idzatu, unditembererere anthu awa.
Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Kodi sindinatumize kwa iwe ndithu kukakuitana? Unalekeranji kudza kwa ine? Sindikhoza kodi kukuchitira ulemu?
Ndipo akulu a Mowabu ndi akulu a Midiyani anamuka ndi mphotho za maula m'dzanja lao; anadza kwa Balamu, nanena naye mau a Balaki.
Chifukwa chake thawira ku malo ako tsopano; ndikadakuchitira ulemu waukulu; koma, taona, Yehova wakuletsera ulemu.