Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.
Danieli 2:30 - Buku Lopatulika Koma ine, chinsinsi ichi sichinavumbulutsidwe kwa ine chifukwa cha nzeru ndili nayo yakuposa wina aliyense wamoyo, koma kuti kumasuliraku kudziwike kwa mfumu, ndi kuti mudziwe maganizo a mtima wanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ine, chinsinsi ichi sichinavumbulutsidwa kwa ine chifukwa cha nzeru ndili nayo yakuposa wina aliyense wamoyo, koma kuti kumasuliraku kudziwike kwa mfumu, ndi kuti mudziwe maganizo a mtima wanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma chinsinsi ichi chavumbulutsidwa kwa ine, si chifukwa chakuti ndili ndi nzeru zochuluka kuposa anthu ena onse, koma kuti mfumu mudziwe tanthauzo la maloto anu ndi kuti muzindikire maganizo amene anali mu mtima mwanu. |
Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.
Ndakuitana iwe dzina lako, chifukwa cha Yakobo mtumiki wanga ndi Israele wosankhidwa wanga; ndakuonjezera dzina, ngakhale iwe sunandidziwe Ine.
Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa chidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Daniele anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse.
Mfumu inamyankha Daniele, niti, Zoona Mulungu wako ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa mafumu, ndi wovumbulutsa zinsinsi; popeza wakhoza kuvumbulutsa chinsinsi ichi.
Pamenepo Daniele anapempha mfumu, ndipo anaika Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, ayang'anire ntchito za dera la ku Babiloni. Koma Daniele anakhala m'bwalo la mfumu.
Pakuti taona, Iye amene aumba mapiri, nalenga mphepo, nafotokozera munthu maganizo ake, nasanduliza m'mawa ukhale mdima, naponda pa misanje ya dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova Mulungu wa makamu.
Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense: koma chifukwa cha osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.
Ndipo Ambuye akadapanda kufupikitsa masikuwo, sakadapulumuka munthu mmodzi yense; koma chifukwa cha osankhidwa amene anawasankha, anafupikitsa masikuwo.
Koma m'mene Petro anachiona, anayankha kwa anthu, Amuna inu a Israele, muzizwa naye bwanji ameneyo? Kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamyendetsa iye ndi mphamvu ya ife eni, kapena ndi chipembedzo chathu?
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
Pakuti zonsezi nza kwa inu, kuti chisomocho, chochulukitsidwa mwa unyinjiwo, chichulukitsire chiyamiko ku ulemerero wa Mulungu.