Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 3:12 - Buku Lopatulika

12 Koma m'mene Petro anachiona, anayankha kwa anthu, Amuna inu a Israele, muzizwa naye bwanji ameneyo? Kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamyendetsa iye ndi mphamvu ya ife eni, kapena ndi chipembedzo chathu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Koma m'mene Petro anachiona, anayankha kwa anthu, Amuna inu a Israele, muzizwa naye bwanji ameneyo? Kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamyendetsa iye ndi mphamvu ya ife eni, kapena ndi chipembedzo chathu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Pamene Petro adaona zimenezi, adalankhula nawo anthuwo, adati, “Inu Aisraele, bwanji mukuzizwa ndi zimenezi? Bwanji mukutiyang'ana ngati kuti tamuyendetsa munthuyu ndi mphamvu zathuzathu? Kodi mukuyesa kuti nchifukwa choti ndife opembedza Mulungu kopambana?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Petro ataona zimenezi anawawuza kuti, “Inu Aisraeli, chifukwa chiyani mukudabwa ndi zimene zachitikazi? Bwanji mukuyangʼana ife ngati kuti tamuyendetsa munthuyu ndi mphamvu yathu kapena chifukwa cha kupembedza kwathu?

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 3:12
15 Mawu Ofanana  

Ndipo iwo anati kwa iye, Ife talota maloto, ndipo tilibe wotimasulira. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Kodi Mwini kumasulira si ndiye Mulungu? Mundifotokozeretu.


Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.


Iye wolankhula zochokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha. Iye wakufuna ulemu wa Iye amene anamtuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.


Amuna, abale, ana a mbadwa ya Abrahamu, ndi iwo mwa inu akuopa Mulungu, kwa ife atumidwa mau a chipulumutso ichi.


Amuna inu Aisraele, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa Iye pakati pa inu monga mudziwa nokha;


Koma m'mene anagwira Petro ndi Yohane, anawathamangira pamodzi anthu onse kukhonde lotchedwa la Solomoni, alikudabwa ndithu.


Mulungu wa Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wake Yesu; amene inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula.


Chifukwa chake ndinena, Mulungu anataya anthu ake kodi? Msatero ai. Pakuti inenso ndili Mwisraele, wa mbeu ya Abrahamu, wa fuko la Benjamini.


ndiwo Aisraele; ali nao umwana, ndi ulemerero, ndi mapangano, ndi kupatsa kwa malamulo, ndi kutumikira mu Kachisi wa Mulungu, ndi malonjezo;


si kuti tili okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu;


Ndipo mmodzi wa akulu anayankha, nanena ndi ine, Iwo ovala zovala zoyera ndiwo ayani, ndipo achokera kuti?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa